Jeremiah 16:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Ine ndidzakupirikitsani m'dziko lino ndi kukuloŵetsani m'dziko limene inu ndi makolo anu simulidziŵa. Kumeneko mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, chifukwa Ine sindidzakuchitiraninso chifundo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake ndidzakutulutsani inu m'dziko muno munke kudziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu ina usana ndi usiku, kumene sindidzachitira inu chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.