Jeremiah 16:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵalanga moŵirikiza, chifukwa cha kuipa kwao ndi machimo ao. Ndidzatero chifukwa chakuti aipitsa dziko langa ndi mafano ao amene ali ngati mitembo, ndipo dziko limene lili choloŵa changa adalidzaza ndi mafano ao onyansa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi cimo lao cowirikiza; cifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza colowa canga ndi zonyansa zao.