Jeremiah 16:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, ndinu mphamvu zanga ndi linga langa, ndinu pothaŵira panga pa nthaŵi ya mavuto. Anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu kuchokera ku malire onse a dziko lapansi. Adzati, “Makolo athu anali ndi milungu yonama, anali ndi mafano achabechabe opanda phindu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa, pothawirapo panga nthawi ya masautso, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti, “Makolo anthu anali ndi milungu yonama, anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira colowa ca bodza lokha, zopanda pace ndi zinthu zosapindula nazo.