Jeremiah 16:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Nchifukwa chake ndidzaŵaphunzitsa, ndidzaŵaphunzitsa kokha kano kuti adziŵe mphamvu zanga zopambana. Ndithudi adzadziŵa kuti Ine dzina langa ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho Ine ndidzawaphunzitsa, kokha kano kuti adziwe za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga. Pamenepo adzadziwa kuti dzina langa ndi Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.