Jeremiah 16:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
onsewo adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzaŵalira maliro kapena kuŵaika m'manda. Adzakhala ngati ndoŵe yotayikira pansi. Ena adzafera pa nkhondo, ena adzafa ndi njala. Ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakuthengo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za kumlengalenga, ndi zilombo za dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za kumlengalenga, ndi zirombo za dziko lapansi.