Jeremiah 16:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe, onsewo adzafa m'dziko lino. Koma maliro ao sadzaikidwa, iwowo sadzaŵalira. Palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi chifukwa cha malirowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akulu ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzachita maliro ao, sadzadzicheka, sadzadziyeseza adazi, chifukwa cha iwo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo;