Jeremiah 16:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pa nthaŵi yanu yomwe, ndiponso pa malo omwe ano ndidzathetsa mau achisangalalo ndi achimwemwe, ndipo ndidzachotsa liwu la mkwati wamwamuna ndi la mkwati wamkazi inuyo mukuwona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwitibwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi.