Jeremiah 17:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire. Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera, ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa cuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ace cidzamsiya iye, ndipo pa citsirizo adzakhala wopusa.