Jeremiah 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, amene Aisraele amagonera pa Inu, onse okukanani adzaŵachititsa manyazi. Onse okusiyani adzafafanizika ngati maina olembedwa pa dothi, chifukwa chokana Chauta, kasupe wa madzi opatsa moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli, onse amene amakusiyani adzachita manyazi. Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi chifukwa anakana Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu Yehova, ciyembekezo ca Israyeli, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondicokera Ine adzalembedwa m'dothi, cifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.