Jeremiah 17:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine sindidakukakamizeni kuti mufikitse zovuta. Mukudziŵa kuti tsiku la tsoka sindinkalilakalaka. Zonse zimene ndidalankhula mukuzidziŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kuchokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, chimene chinatuluka pa milomo yanga chinali pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange. Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka. Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kucokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, cimene cinaturuka pa milomo yanga cinali pamaso panu.