Jeremiah 17:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ondizunza ndiwo achite manyazi, osati ineyo. Ade nkhaŵa ndi iwowo, osati ineyo. Tsiku la tsoka liŵafikire, ndipo muŵaononge kotheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la choipa, muwaononge ndi chionongeko chowirikiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ondizunza anga achite manyazi, koma musandichititse manyazi; iwo achite mantha kwambiri, koma ine mundichotsere manthawo. Tsiku la mavuto liwafikire; ndipo muwawononge kotheratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la coipa, muwaononge ndi cionongeko cowirikiza.