Jeremiah 17:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukaime pa chipata chachikulu chodzerapo anthu ambiri, chimene mafumu a ku Yuda amaloŵerapo ndi kutulukirapo. Upitenso ku zipata zonse za Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'chipata cha ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene atulukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'cipata ca ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene aturukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;