Jeremiah 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chonsecho ana ao amakumbukira maguwa ao aja ndi zoimiritsa zao zansembe, patsinde pa mtengo wogudira uliwonse, pa mapiri am'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao kumitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ana awo amakumbukira maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera, pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri, pa mapiri aatali mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao ku mitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitari.