Jeremiah 17:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musanyamule katundu aliyense kutuluka naye m'nyumba mwanu, kapena kugwira ntchito iliyonse pa Sabata. Koma muzilisunga tsiku la Sabatalo kuti likhale lopatulika, monga ndidalamulira makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
musatulutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire ntchito ili onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;