Jeremiah 17:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta akunena kuti, “Koma inu muzindimvera Ine, ndi kuleka kunyamula katundu kapena kumatuluka naye pa zipata za mzinda uno pa Sabata, ndipo muzisunga tsiku la Sabata osagwira ntchito pa tsiku limenelo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala, ngati mundimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira ntchito m'menemo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala, ngati mu ndimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira nchito m'menemo;