Jeremiah 17:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukatsata zimenezi, ndiye kuti pa zipata za mzinda umenewu pazidzaloŵera mafumu odzakhala pa mpando waufumu wa Davide. Azidzaloŵa atakwera pa magareta ndi pa akavalo, ali pamodzi ndi akalonga ao ndi anthu a ku Yuda ndiponso anthu a mu Yerusalemu. Ndipo anthu adzakhazikika mu mzinda umenewu mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala kunthawi zamuyaya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akuru okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera pa magareta ndi akavalo, iwo, ndi akuru ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala ku nthawi zamuyaya.