Jeremiah 17:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adzachokera ku mizinda ya Yuda ndi dziko lonse lozungulira Yerusalemu, dziko la Benjamini, dziko lazidikha, dziko lazitunda, ndiponso ku Negebu, atatenga nsembe zopsereza, nsembe zaufa, nsembe zalubani, ndiponso nsembe zothokozera, kupita nazo ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzachokera kumidzi ya Yuda, ndi kumalo akuzungulira Yerusalemu, ndi kudziko la Benjamini, ndi kuchidikha, ndi kumapiri, ndi kumwera, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi lubani, ndi kudza nazo zamayamikiro, kunyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzacokera ku midzi ya Yuda, ndi ku malo akuzungulira Yerusalemu, ndi ku dziko la Benjamini, ndi kucidikha, ndi kumapiri, ndi ku Mwela, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi zonunkhira, ndi kudza nazo zamiyamikiro, ku nyumba ya Yehova.