Jeremiah 17:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mukapanda kundimvera, mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika, ndipo mukamanyamula katundu aliyense nkumakaloŵa pa zipata za Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ndiye kuti ndidzazitentha zipata zimenezo. Moto udzapsereza nyumba zaufumu za ku Yerusalemu, moto wake wosazimika.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zakezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zacezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.