Jeremiah 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Woteroyo adzakhala ngati chitsamba m'chipululu, ndipo sadzapeza zabwino. Adzakhala m'chipululu mopanda madzi, m'dziko lamchere m'mene anthu sangathe kukhalamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'chipululu, ndipo saona pamene chifika chabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'chipululu, dziko lachikungu lopanda anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu; iye sadzapeza zabwino. Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi, mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'cipululu, ndipo saona pamene cifika cabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'cipululu, dziko lacikungu lopanda anthu.