Jeremiah 17:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m'mphepete mwa mtsinje, umene umatambalitsa mizu yake m'mbali mwa madzi. Suwopa kukamatentha, chifukwa masamba ake safota. Pa chaka chachilala sukuda nkhaŵa, ndipo suleka kubala zipatso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje. Mtengowo suopa pamene kukutentha; masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse. Suchita mantha pa chaka cha chilala ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.