Jeremiah 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma mtunduwo nkumapitiriza kuchita zoipa pamaso panga, osamvera mau anga, ndiye kuti sindidzauchitira zabwino zimene ndidaati ndiwuchitire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma ukacita coipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka cabwinoco, ndidati ndiwacitire.