Jeremiah 18:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pita tsono, ukauze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti Chauta akuti, Ine ndikukonzekera zoti ndikuchiteni, ndikuganiza zoti ndikulangeni. Bwererani nonse, aliyense aleke njira zake zoipa. Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu choipa, ndilingalira inu kanthu kakuchitira inu choipa; mubwerere tsono inu nonse, yense kunjira yake yoipa, nimukonze njira zanu ndi machitidwe anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano nenatu kwa anthu a Yuda, ndi kwa okhala m'Yerusalemu, kuti, Atero Yehova: Taonani, Ine ndipangira inu coipa, ndilingalira inu kanthu kakucitira inu coipa; mubwerere tsono inu nonse, yense ku njira yace yoipa, nimukonze njira zanu ndi macitidwe anu.