Jeremiah 18:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nzopanda pake. Tidzachita monga m'mene tifunira, ndipo aliyense mwa ife azidzangotsata zoipa za mtima wake wokanika.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iwo ati, Palibe ciyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzacita yense monga mwa kuuma kwa mtima wacewoipa.