Jeremiah 18:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ukafunse anthu a mitundu ina yonse, ngati alipo amene adamvapo zotere. Israele amene adaali ngati namwali wosadziŵa mwamuna wachita chinthu choipa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Uwafunse anthu a mitundu ina kuti: Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi? Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita chinthu choopsa kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israyeli wacita cinthu coopsetsa kwambiri.