Jeremiah 18:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ai, komabe anthu anga andiiŵala. Amafukizira lubani mafano opanda pake. Amakhumudwa m'njira zao zakale. Amayenda m'njira zodzera m'thengo, kusiya mseu wabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pake; aphunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale, kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu anthu anga andiyiwala; akufukiza lubani kwa mafano achabechabe. Amapunthwa mʼnjira zawo zakale. Amayenda mʼnjira zachidule ndi kusiya njira zabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakun anthu anga andiiwala Ine, afukizira zopanda pace; apunthwitsa iwo m'njira zao, m'njira zakale kuti ayende m'njira za m'mbali, m'njira yosatundumuka;