Jeremiah 18:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lao amalisandutsa lochititsa nyansi ndi lodzetsa mfuu wa mantha mpaka muyaya. Aliyense wodutsamo adzakhala akudabwa ndi kumapukusa mutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti aliyense dziko lao likhale lodabwitsa, ndi kutsonya chitsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lawo amalisandutsa chipululu, chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse; onse odutsapo adzadabwa kwambiri ndipo adzapukusa mitu yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti aliyese dziko lao likhale lodabwitsa, ndi: kutsonya citsonyere; yense wakupitapo adzadabwa, ndi kupukusa mutu wace.