Jeremiah 18:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi choipa chingakhale dipo la chinthu chabwino? Komabe andikumbira dzenje. Kumbukirani kuti paja ndidaabwera kwa Inu kudzaŵapempherera kuti muleke kuŵakwiyira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino? Komabe iwo andikumbira dzenje. Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu kudzawapempherera kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi coipa cibwezedwe pa cabwino? pakuti akumbira moyo wanga dzenje, Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwacotsera iwo ukali wanu.