Jeremiah 18:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake mulange ana ao ndi njala. Muŵaononge ndi nkhondo. Akazi ao akhale amasiye, opanda ana. Amuna ao afe ndi mliri, anyamata ao afe ndi lupanga ku nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho langani ana awo ndi njala; aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga. Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye; amuna awo aphedwe ndi mliri, anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo ku mphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.