Jeremiah 18:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mukudziŵadi ziwembu zao zonse zofuna kundipha. Musaŵakhululukire zolakwa zao, ndithu, musaŵachotsere machimo ao. Agonjetsedwe pamaso panu, ndipo muŵalange muli okwiya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize tchimo lao pamaso panu; aphunthwitsidwe pamaso panu; muchite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Inu Yehova, mukudziwa ziwembu zawo zonse zofuna kundipha. Musawakhululukire zolakwa zawo kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu. Agonjetsedwe pamaso panu; muwalange muli wokwiya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma, Yehova, mudziwa uphungu wao wonse wakundinenera ine kundipha ine; musakhulukire mphulupulu yao, musafafanize cimo lao pamaso panu; apunthwitsidwe pamaso panu; mucite nao m'nthawi ya mkwiyo wanu.