Jeremiah 18:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chiŵiya chimene ankaumbacho chitakhala chopotoka pomalinga ndi kaumbidwe kake kolakwika, iye uja ankaumbanso chiŵiya china ndi dothi lomwelo, monga ankafunira mwiniwakeyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mbiya alikuiumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya ina, monga kunamkomera woumba kuiumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mbiya alikulumba ndi dothi inaonongeka m'dzanja la woumba, anaiumbanso mbiya yina, monga kunamkomera woumba kulumba.