Jeremiah 18:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Inu Aisraele, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira woumba mbiya? Zedi, inuyo muli m'manja mwangamu monga momwe umakhalira mtapo m'manja mwa woumba mbiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyumba ya Israele inu, kodi sindingathe kuchita ndi inu monga woumba uyu? Ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyumba ya Israyeli inu, kodi sindingathe kucita ndi inu monga woumba uyu? ati Yehova. Taonani, monga dothi m'dzanja la woumba, momwemo inu m'dzanja langa, nyumba ya Israyeli.