Jeremiah 19:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, Umu ndi m'mene ndidzaonongere anthu ameneŵa, monga momwe woumba amaphwanyira mbiya yake, kotero kuti sangathenso kuikonza. Anthu akufawo adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti kwina kulikonse sikudzakhala malo oŵaika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Chomwecho ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kuiumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Comweco ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kulumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.