Jeremiah 19:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumba za ku Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti, chifukwa ndizo nyumba zimene pa madenga ao ankaotcherapo nsembe kwa milungu ya mumlengalenga, namapereka nsembe yazakumwa kwa milungu ina.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu yina nsembe zothira.