Jeremiah 19:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Yeremiya adabwerako ku Tofeti kumene Chauta adaamtuma kuti akalose, naimirira m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo adauza anthu onse kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Yeremiya anadza kuchokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Yeremiya anadza kucokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse: