Jeremiah 19:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndidzagwetsa tsoka pa mzinda uwu pamodzi ndi pa midzi yake yonse monga ndidaanenera, chifukwa choti anthu ake ndi okanika, ndipo akukana kumvera mau anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yake yonse choipa chonse chimene ndaunenera; chifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yace yonse coipa conse cimene ndaunenera; cifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.