Jeremiah 19:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukanene kuti, Inu mafumu a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu, imvani mau a Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ndidzagwetsa tsoka loopsa pa malo ano, kotero kuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzatengera malo ano choipa, chimene aliyense adzachimva, makutu ake adzachita woo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera malo ano coipa, cimene ali yense adzacimva, makutu ace adzacita woo.