Jeremiah 19:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu andikana Ine, ndipo aipitsa malo ano. Akhala akufukiza lubani kwa milungu yachilendo imene iwowo, makolo ao ndiponso mafumu a ku Yuda sadaidziŵe. Ndipo pa malo ano adakhetserapo magazi a anthu osachimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;