Jeremiah 19:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauza, sindinachinena, sichinalowa m'mtima mwanga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, cimene sindinawauza, sindinacinena, sicinalowa m'mtima mwanga;