Jeremiah 19:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Anthu am'menemo ndidzaŵaphetsa kwa adani ao ku nkhondo, ndipo ndidzaŵakanthitsa kwa anthu oŵazonda. Mitembo yao ndidzaisandutsa chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo za pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale chakudya cha mbalame za m'mlengalenga, ndi cha zilombo za dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale cakudya ca mbalame za m'mlengalenga, ndi ca zirombo za dziko lapansi.