Jeremiah 19:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaumiriza anthuwo kuti adye ana ao omwe aamuna ndi aakazi. Adzadyana choncho pa nthaŵi yoopsa pamene adzazingidwa ndi adani ao ofuna kuŵazunza.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao aamuna ndi aakazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wake, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao amuna ndi akazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wace, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.