Jeremiah 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu ina ambangulira ndi kumuwopsa ngati mikango. Dziko lake alisandutsa chipululu. Mizinda yake adaiwononga, idasanduka mabwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, midzi yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani ake abangulira ndi kumuopseza ngati mikango. Dziko lake analisandutsa bwinja; mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lace, midzi yace yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.