Jeremiah 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga tsopano mudzapindulanji mukadzapita ku Ejipito, kukamwa madzi a m'Nailo? Mudzapeza phindu lanji mukadzapita ku Asiriya kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano uli nacho chiyani m'njira ya ku Ejipito, kumwa madzi a Sihori? Uli nacho chiyani m'njira ya ku Asiriya, kumwa madzi a m'mtsinje?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto, kukamwa madzi a mu Sihori? Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya, kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano uli naco ciani m'njira ya ku Aigupto, kumwa madzi a Sihori? uli naco ciani m'njira ya ku Asuri, kumwa madzi a m'Nyanja?