Jeremiah 2:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzalangidwa ndi machimo anu omwe: poti mwandikana, ndidzakuimbani mlandu. Muganizire bwino za kuipa kwake kwa kundisiya Ine, Chauta, Mulungu wanu. Mulingalire kuŵaŵa kwake kwa kukhala osandiwopa,” akuterotu Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Choipa chako dzidzakulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ichi ndi choipa ndi chowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyipa kwanuko kudzakulangani; kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani. Tsono ganizirani bwino, popeza ndi chinthu choyipa kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu; ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu. Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Coipa cako cidzai kulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ici ndi coipa ndi cowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.