Jeremiah 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kuyambira masiku amakedzana inu mudathyola goli lanu ndi kudula nsinga zanu. Mudati, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithu inu mwakhala ngati mkazi wadama, mukupembedza milungu ina pochita zadama pa phiri lililonse ndiponso pansi pa mtengo wogudira uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kale lomwe ndinathyola goli lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitali, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kuchita dama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu ndi kudula msinga zanu; munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’ Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere. Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kale lomwe ndinatyola gori lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitari, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kucita dama.