Jeremiah 2:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Uneneranji kuti, ‘Ine sindidadziipitse, sindidatsate Baala?’ Kumbukira m'mene udachimwira m'chigwamo, zindikira zimene wachita. Wakhala ngati ngamira yaikazi, yothamanga uku ndi uku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse; sindinatsatire Abaala’? Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja; zindikira bwino zomwe wachita. Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro yomangothamanga uku ndi uku,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'cigwa, dziwa cimene wacicita; ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m'njira zace;