Jeremiah 2:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Banja la Israele lidzachita manyazi, monga momwe mbala imachitira manyazi akaigwira. Aisraele, mafumu ao ndi akalonga ao, ansembe ao ndi aneneri ao, onsewo adzachita manyazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mbala ili ndi manyazi pamene igwidwa, chomwecho nyumba ya Israele ili ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa, moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi; Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo, ansembe ndi aneneri awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga mbala iri ndi manyazi pamene igwidwa, comweco nyumba ya Israyeli iri ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akuru ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;