Jeremiah 2:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amauza mtengo kuti ‘Iwe ndiwe bambo wathu,’ amauza mwala kuti ‘Iwe ndiwe amene udatibala.’ Koma Ine amandifulatira, m'malo motembenukira kwa Ine. Tsono akakhala pa mavuto amati, ‘Dzambatukani, mutithandize.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’ ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’ Iwo andifulatira Ine, ndipo safuna kundiyangʼana; Koma akakhala pa mavuto amati, ‘Bwerani mudzatipulumutse!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kubvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.