Jeremiah 2:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga milungu yanu ili kuti, milungu ija mudadzipangira ija? Idzambatuketu, ngati ingathe kukupulumutsani pa nthaŵi yanu ya mavuto. Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri, kuchuluka kwake monga momwe iliri mizinda yanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ili kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kuvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kuchuluka kwa midzi yako, Yuda iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha? Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani pamene muli pamavuto! Inu anthu a ku Yuda, milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iri kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kubvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, Yuda iwe.