Jeremiah 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Israele udaali wopatulika wa Chauta. Udaali ngati chipatso chake choundukula. Ndidaika zoŵaŵa ndi mavuto aakulu, pa onse amene adakuzunza, ndipo tsoka linkaŵagwera,” akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli anali wopatulika wa Yehova, anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola; onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa ndipo mavuto anawagwera,’ ” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Israyeli anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zace; onse amene adzamudya iye adzayesedwa oparamula; coipa cidzawagwera, ati Yehova.