Jeremiah 2:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu anthu amakono, imvani mau a Chauta. “Kodi ndakhala ngati chipululu kwa Israele, kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani tsono anthu anga akunena kuti, ‘Ndife mfulu, sitidzabweranso kwa Inu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova: “Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli kapena ngati dziko la mdima wandiweyani? Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda; sitidzabweranso kwa Inu’?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israyeli cipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Cifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?